Deuteronomy 28:57 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.