Deuteronomy 28:58 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;