Deuteronomy 28:62 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mudaachuluka ngati nyenyezi zakuthambo, koma amoyo mudzakhala ochepa, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mukacuruka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu.