Deuteronomy 28:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simudzapeza mtendere kwina kulikonse ndipo malo anuanu simudzaŵapeza. Mudzakhala ankhaŵa, osoŵa thandizo ndi otaya mtima, ndipo Chauta ndiye adzagwetse zimenezi pa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.