Deuteronomy 28:67 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitima yanu idzakhala yamantha poona kalikonse. M'maŵa mulimonse muzidzangofuna kuti kude. Madzulo aliwonse muzidzafuna kuti kuche.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m'mawa! Chifukwa cha mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! ndi madzulo mudzati, Mwenzi utafika m'mawa! cifukwa ca mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi cifukwa ca zopenya maso anu zimene mudzazipenya.