Deuteronomy 28:68 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adzakutumizaninso ku Ejipito m'zombo zapanyanja, ngakhale kuti ndidaalonjeza kuti simudzapitakonso. Kumeneko mudzayesayesa kudzigulitsa ngati akapolo kwa adani anu, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kukugulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogulainu.