Deuteronomy 28:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace.