Deuteronomy 29:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aŵa ndi mau a chipangano chimene Chauta adalamula Mose kuti achite ndi Aisraele m'dziko la Mowabu. Mau achipangano ameneŵa adangoonjezeka pa mau aja achipangano amene Chauta adaachita ndi iwowo ku phiri la Horebu kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao m'Horebu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndiwo mawu a mʼpangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisraeli ku Mowabu, powonjezera pa pangano limene anapangana nawo ku Horebu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi mau a cipangano cimene Yehova analamulira Mose acicite ndi ana a Israyeli m'dziko la Moabu, pamodzi ndi cipanganoco anacita nao m'Horebe.