Deuteronomy 29:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero, mudzakhala anthu a Chauta, ndipo Iyeyo adzakhala Mulungu wanu, monga momwe adalonjezera kwa inu ndi kulumbira kwa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kukukhazikitsani lero lino ngati anthu ake, ndi kuti Iye akhale Mulungu wanu monga anakulonjezani inu ndiponso monga analumbira kwa makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti adzikhazikire inu, mtundu wace wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo.