Deuteronomy 29:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonde muchenjere kuti mwamuna kapena mkazi, ngakhale banja, kaya fuko, kungoti nonsenu amene muli pano lero lino, musapotoloke kuti muchoke kwa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumapembedza milungu ya anthu a mitundu ina. Kuteroko kungofanafana ndi muzu umene umati ukakula, umasanduka chiphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onetsetsani kuti pasapezeke mwamuna kapena mkazi, banja kapena fuko pakati panu lero amene mtima wawo udzapandukira Yehova Mulungu wanu ndi kupita kukapembedza milungu ya mitundu iyo. Onetsetsani kuti pasapezeke muzu pakati panu wotulutsa mankhwala akupha otere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena pfuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi cowawa.