Deuteronomy 29:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonde muchenjere kuti pasakhale wina pano lero, womva mau ameneŵa, komabe namanena mumtima mwake kuti zinthu zidzamuyenderabe bwino, ngakhale akhale wokanika chotani nkumachita zake. Zimenezi zidzangoputira nonsenu chiwonongeko, abwino ndi oipa omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wotere akamva mawu a lumbiro ili, asadzidalitse yekha mʼmaganizo mwake namati, “Ine ndidzapulumuka ngakhale nditapitiriza kuyenda njira yanga.” Zoterezi zidzadzetsa masautso pa nthaka ya chinyontho ndi yowuma yomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwace, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;