Deuteronomy 29:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wotere Chauta sadzamkhululukira. Ndithu Chauta adzamkwiyira ndi nsanje yoyaka. Matemberero olembedwa m'buku muno adzamgwera ndipo Chauta adzamuwonongeratu ndipo adzaiŵalika pa dziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova sadzamukhululukira. Mkwiyo ndi nsanje ya Yehova zidzamuyakira munthuyo. Matemberero onse wolembedwa mʼbukuli adzamugwera iye ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yace zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lace pansi pa thambo.