Deuteronomy 29:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mibadwo yanu yakutsogolo, monga zidzukulu zanu ndi alendo ochokera kutali, adzaŵapenya masoka amenewo, pamodzi ndi masautso amene Chauta adzagwetse pa dziko lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana anu a mibado yakutsogolo ndi alendo amene adzachokera kutali adzaona matsoka amene adzakugwerani mʼdziko muno ndiponso matenda amene Yehova adzabweretsa pa dzikoli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wocokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi; Yehova awadwalitsa nazo,