Deuteronomy 29:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Minda yanu idzakhala yoguga, yodzaza ndi sulufule ndi mchere. M'minda imeneyo simudzamera kalikonse, ngakhale ndi udzu womwe. Dziko lanu lidzakhala ngati mizinda ija ya Sodomu ndi Gomora, ndiponso ya ku Adima ndi Zoboimu, imene Chauta adaononga pa nthaŵi imene anali wokwiya koopsa ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lonse lidzasanduka nthaka ya mchere ndi ya sulufule. Simudzadzalamo kanthu, simudzakhala chomera chilichonse, ndi mbewu yomera mʼmenemo. Dziko lanu lidzakhala lowonongeka ngati Sodomu ndi Gomora, Adima ndi Zeboimu, mizinda imene Yehova anayiwononga ndi mkwiyo wake waukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti lidapsa dziko lace lonse ndi sulfure, ndi mcere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwace kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wace ndi ukali wace;