Deuteronomy 29:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yankho la mafunso onseŵa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chake nchakuti anthuŵa adaphwanya chipangano chimene adachita ndi Chauta, Mulungu wa makolo ao, nthaŵi imene Iyeyo adaŵatulutsa ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo yankho la mafunso amenewa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chakuti anthu awa aphwanya pangano la Yehova Mulungu wa makolo awo, pangano limene Iye anapangana nawo pamene anawatulutsa ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo adzati, Popeza analeka cipangano ca Yehova, Mulungu wa makolo ao, cimene anacita nao pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto;