Deuteronomy 29:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munalibe buledi woti muzidya, ngakhalenso vinyo kapena chakumwa chaukali, koma Chauta adakupatsani zonse zokusoŵani, kuti mudziŵe kuti Iye ndi Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena chakumwa cholimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu simunadye buledi ndi kumwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa. Ndinachita izi kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena cakumwa colimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.