Deuteronomy 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Ogi yekha, mfumu ya ku Basani, ndiye amene adatsala mwa Arefaimu. Kama lake linali lachitsulo, m'litali mwake linali la mamita anai, muufupi mwake mamita aŵiri, polinganiza ndi miyeso ya nthaŵi imeneyo. Kamalo angathe kuchiwonabe ku Raba, mzinda wa Aamoni.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi m'Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
(Pakuti Ogi mfumu ya Basana anatsala yekha wa iwo otsalira Arefai; taonani, kama wace ndiye kama wacitsulo; sukhala kodi m'Raba wa ana a Amoni? utali wace mikono isanu ndi inai, kupingasa kwace mikono inai, kuyesa mkono wa munthu.)