Deuteronomy 3:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzikolo titalanda, ndidagaŵira fuko la Rubeni ndi la Gadi dera lija kuyambira ku Aroere, pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, ndiponso theka la dziko lamapiri la Giliyadi, pamodzi ndi mizinda yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi midzi yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroeri, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Gileadi, ndi midzi yace, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.