Deuteronomy 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yairi, wa fuko la Manase, adatenga dera lonse la Arigobu, ndiye kuti Basani, mpaka kukafika ku malire a Gesuri ndi Maaka. Mizindayo adaitchula dzina lake, ndipo mpaka lero lino, imadziŵika kuti ndi ya Yairi.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobi, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalicha dzina lace, Basana Haroti Yairi, kufikira lero lino.)