Deuteronomy 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lonse kuchokera ku Giliyadi mpaka ku chigwa cha Arinoni, ndidapatsa fuko la Rubeni ndi la Gadi. Pakatimpakati pa chigwa cha Arinoni ndiye panali malire akumwera, ndipo malire ake akumpoto anali mtsinje wa Yaboki, umene mbali yake inali malire a dziko la Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Gileadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa cigwa ndi malire ace, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;