Deuteronomy 3:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakuzambwe dziko lao linkafika mpaka ku mtsinje wa Yordani, kuchokera ku Kinereti kumpoto, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja yamchere kumwera. Ndipo chakuvuma linkafika pa tsinde la phiri la Pisiga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi cidikha, ndi Yordano ndi malire ace, kuyambira ku Kinerete kufikira ku nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa.