Deuteronomy 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo ndidaakulamulani kuti, “Chauta, Mulungu wathu, ndiye wakupatsani dzikoli kuti likhale lanu. Amuna onse otha kumenya nkhondo atenge zida ndipo atsogolere abale anu, mafuko a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanu lanu, muoloke, amuna onse amphamvu obvala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israyeli.