Deuteronomy 3:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵathandize Aisraele anzanu mpaka akhazikike mwamtendere m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu waŵapatsa kuzambwe kwa Yordani, monga momwe Chauta adakuchitirani inu. Pambuyo pake aliyense mwa inu adzabwere ku dera limene ndidakupatsani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lila la Yordano; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku colowa cace, cimene ndinakupatsani.