Deuteronomy 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Ambuye Chauta, mwangondiwonetsa chiyambi chake chokha cha ntchito za ukulu wanu ndi mphamvu zanu. Kumwambako, ngakhalenso pansi pano, palibe Mulungu wina amene angathe kuchita zinthu zamphamvu zonga zimene inu mumachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakucita monga mwa nchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?