Deuteronomy 3:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta anali wondikwiyira ine chifukwa cha inu, ndipo sadandimvere konse. M'malo mwake adangoti, “Pakwana! Usanenenso zimenezi!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova anakwiya ndi ine, cifukwa ca inu, sanandimvera ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Cikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za cinthuci.