Deuteronomy 3:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma umlangize bwino Yoswayu ndi kumlimbitsa mtima, chifukwa iyeyu ndiye atsogolere anthuŵa kuwoloka mpaka tsidya linalo, ndi kukakhala m'dziko limene udzaliwonalo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma langiza Yoswa, dioloketu numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale lao lao.