Deuteronomy 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidaononga midziyo ndi mizinda yonse, ndipo tidapha onse amuna ndi akazi ndi ana omwe, monga momwe tidachitira mizinda ya mfumu Sihoni wa ku Hesiboni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinachitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse midzi yonse, amuna, akazi ndi ana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinacitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse midzi yonse, amuna, akazi ndi ana.