Deuteronomy 30:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m'buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m'buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ace ndi malemba ace olembedwa m'buku la cilamulo ici; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.