Deuteronomy 30:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kusunga malamulo ace ndi malemba ace ndi maweruzo ace, kuti mukakhale ndi moyo ndi kucuruka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.