Deuteronomy 30:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ace, ndi kummamatira iye, tr pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ocuruka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.