Deuteronomy 30:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta, Mulungu wanu, adzakukhazikaninso pabwino ndi kukuchitirani chifundo. Adzakusokolotsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu, kumene adakumwaziraniko, ndipo adzakusandutsaninso olemera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzaucotsa ukapolo wanu, ndi kukucitirani cifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.