Deuteronomy 30:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakuperekezani ku dziko limene makolo anu anali nalo kale, kuti mukakhazikikeko ndinu. Ndipo adzakupezetsani bwino ndi kukuchulukitsani kopambana m'mene adaaliri makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala laolao la makolo anu, nilidzakhala lanulanu; ndipo adzakuchitirani zokoma, ndi kukuchulukitsani koposa makolo anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala lao lao la makolo anu, nilidzakhala lanu lanu; ndipo adzakucitirani zokoma, ndi kukucurukitsani koposa makolo anu.