Deuteronomy 30:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani inu ndi zidzukulu zanu mtima womvera, kotero kuti muzidzamkonda ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Motero mudzakhalabe ndi moyo m'dziko limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.