Deuteronomy 31:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sonkhanitsan; anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici;