Deuteronomy 31:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa njira imeneyi zidzukulu zanu zimene sizidamve malamulo a Chauta nkale lomwe, zidzamva, ndipo zidzaphunzira kuwopa Chauta nthaŵi yonse imene zidzakhale m'dziko limene mukukakhalamolo patsidya pa Yordani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti ana ao osadziwa amve, oaphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu.