Deuteronomy 31:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Nthaŵi ya moyo wako yatsala yochepa. Itana Yoswa, ubwere naye ku chihema chamsonkhano kuti ndimulangize.” Mose pamodzi ndi Yoswa adapita ku chihema chamsonkhano,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Nthawi ya kufa kwako yafika. Itana Yoswa ndipo mubwere ku tenti ya msonkhano, kumene Ine ndidzamulangiza.” Choncho Mose ndi Yoswa anabwera ku tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'cihema cokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'cihema cokomanako.