Deuteronomy 31:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Patsala pang'ono kuti iwe umwalire. Ndiye iwe ukapita, anthuŵa adzaphwanya chipangano chomwe ndidachita nawo. Adzandisiya Ine, nkumapembedza milungu ya dziko limene akukakhalamolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, “Iwe ukupita kukapuma kumene kuli makolo ako, ndipo ukangomwalira, anthu awa adzayamba kupembedza milungu yachilendo ya mʼdziko limene akukalowamo. Adzanditaya ndi kuphwanya pangano lomwe ndinachita nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, oadzatsata ndi cigololo milungu yacilendo ya dziko limene analowa pakati pace, nadzanditava Ine, ndi kutyola cipangano canga ndinapangana naoco.