Deuteronomy 31:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zikadzangotero, ndidzaŵakwiyira ndi kuŵasiya, ndipo adzatheratu. Masoka ndi zoipa zina zambiri zidzaŵagwera. Tsono masiku amenewo azidzanena kuti, ‘Kodi zoipazi sizikutigwera chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wathu, sali nafenso?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zobvuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?