Deuteronomy 31:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵaloŵetsa m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe ndidalonjezera makolo ao. Kumeneko adzapeza chakudya chonse chomwe angachifune, ndipo adzakhala mosangalala. Komabe adzatembenukira ku milungu ina ndi kumaipembedza. Adzandikana Ine, ndipo adzaphwanya chipangano changa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu yina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kutyola cipangano canga.