Deuteronomy 31:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho masoka oopsa adzaŵagwera. Nyimbo imeneyi idzakhala mboni yanga yoŵatsutsa, chifukwa zidzukulu zao zizidzaiimba. Ngakhale tsopano lino ndisanaŵaloŵetse m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzaŵapatsa, ndikudziŵa zimene iwo akulingalira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zobvuta zambiri, nyimbo iyi idzacita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azicita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.