Deuteronomy 31:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova analamula Yoswa mwana wa Nuni kuti, “Khala wamphamvu ndipo limba mtima, chifukwa udzalowetsa Aisraeli mʼdziko limene ndinawalonjeza mwa lumbiro, ndipo Ine mwini ndidzakhala nawe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m'dziko limene ndinawalumbirira: ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.