Deuteronomy 31:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa kukanika kwanu ndiponso uchigaŵenga wanu. Ngati mugalukira Chauta, ndikadali moyo, nanji ndikadzafa, ndiye mudzaposa kugaluka kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova: koposa kotani nanga nditamwalira ine!