Deuteronomy 31:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko pamodzi ndi akuluakulu omwe, kuti ndiŵauze zimenezi. Kumwamba ndi dziko lapansi ndizo zidzakhale mboni zoŵatsutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko anu pamodzi ndi akuluakulu onse, kuti ndiyankhule mawu awa iwo akumva ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni yowatsutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndisonkhanitsire akuru onse a mapfuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kucititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.