Deuteronomy 31:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa kuti ine ndikadzafa, nonse mudzaipa ndipo mudzakana zimene ndakuuzanizi. Koma pambuyo pake kutsogoloko, mudzakomana ndi masoka, chifukwa chochita zoipa pamaso pa Chauta ndi kuputa mkwiyo wake pakuchulukitsa machimo anu. Mwakwiyitsa Chauta pochita zimene Iyeyo amakana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa ndikudziwa kuti ine ndikamwalira mudzayipa kwambiri ndi kutembenuka kuleka njira imene ndinakulamulani. Masiku amene akubwera, masautso adzakugwerani chifukwa mudzachita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuputa mkwiyo wake chifukwa cha zimene manja anu anapanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo cidzakugwerani coipa masiku otsiriza; popeza mudzacita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace ndi nchito za manja anu.