Deuteronomy 31:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwini wake Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakuperekezeni ndi kuwononga mitundu ina yonseyi, kuti inu mukhale m'dziko mwao. Yoswa adzakhala mtsogoleri wanu, monga momwe Chauta wanenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, Iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova.