Deuteronomy 31:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzaŵaononga anthu ameneŵa monga momwe adaonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, pamodzi ndi dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzawacitira monga anacitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.