Deuteronomy 31:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.