Deuteronomy 31:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Mose adaitana Yoswa pamaso pa Aisraele onse ndipo adamuuza kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Ndi iweyo amene udzatsogolere anthu aŵa ku dziko limene Chauta adalonjeza makolo ao. Ndiwe amene udzakhazikitsa anthu m'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israele wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.