Deuteronomy 32:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachita ngati mphungu imene ikuphunzitsa ana ake kuuluka, imene ikungozungulira pamwamba pa ana akewo nitambalitsa mapiko ake, kuti igwire anawo ndi kuŵanyamula pa mapiko ake otambalitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pa mapiko ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chake nʼkumazungulira pamwamba pa ana ake, chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawo ndi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mphungu ikasula cisa cace, Nikapakapa pa ana ace, Iye anayala mapiko ace, nawalandira, Nawanyamula pa mapiko ace;