Deuteronomy 32:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵathandiza kuti azilamula maiko amapiri, ndipo adadya zomera zam'minda. Adaŵadyetsa uchi wam'mathanthwe, ndi mafuta ochokera m'nthaka yamiyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdziko ndi kumudyetsa zipatso za mʼminda. Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe, ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, Ndipo anadya zipatso za m'minda; Namyamwitsa uci wa m'thanthwe, Ndi mafutam'mwala wansangalabwe;